Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 106
Miyambi ya Patsokwe
tinaganiza zoti tikaimangirire pamtengo uwo. Taonani msipu
wake ukungoti biriwiribiriwiri, kukongola. Zoona mbuziyi ife
ndi njala msipu uli m’khonde?” Mwini mbuziyo atamva zimene-
zi anawakhulupiriradi. Koma mbuziyo inkadziwa kuti anthuwo
akunama. Ndiye chifukwa choti sitha kuyankhula, akubawo
anapulumukira m’kamwa mwa mbuzi.
Kuputa ndewu n’kuimirira.
-Munthu amene akufuna kumenyana ndi mnzake amati aka-
yamba mnzake amaimirira kuti amenyane naye. Ukamayamba
kuchita chinthu umafunika kukhala ndi zonse zokwanira kuti
izimalizitse. Ukamawaputa mavuto umafunika kulimba nazo.
Kuputa Vumbwe n’kulinga uli ndi Nkhuku.
-Kuti anthu azikonda kubwera pakhomo umafunika ku-
mawadyetsa bwino. Ukamaputa chinthu umafunika kumakhala
ndi podalira.
Kusadziwa n’kufa komwe.
-Munthu ukakhala mbuli palibe chingakuyendere.
Kusafunsa kudadyetsa njuchi.
-Kufunsa kumathandiza kuti tisakumane ndi mavuto.
Kusafunsa kudamwetsa posamba.
-Kufunsa kumathandiza kuti tisakumane ndi mavuto.
Kusafunsa kudaphikitsa tsabola.
-Kufunsa kumathandiza kuti tisakumane ndi mavuto.
Kusafunsa kudapsetsa Tambala.
-Kufunsa kumathandiza kuti tisakumane ndi mavuto.
Kusalowa m’nyumba salumbira.
-Munthu sunganyanyale kuti sudzachitanso chinthu chomwe
chili chofunika kwambiri pamoyo wako, monga kulowa
m’nyumba mwako.
105