Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 105
Miyambi ya Patsokwe
Kupha Njoka n’kumutu.
-Kupha njoka kumafuna kuimenya mutu. Kuthetsa nkhani
n’kulinga utadziwa chimene chayambitsa.
Kuphera Nkhumba pamsikiti.
-Kuchitira ena zinthu zosayenera komanso zolakwika malinga
ndi chikhalidwe kapena mwambo wawo.
Kuphunzira kumakathera kumanda.
-Pa moyo wa munthu pamakhala zambiri zoti uphunzire ndipo
umaphunzirabe mpaka kudzamwalira. Ena amati kumwalirako
ndi phunzironso palokha. Nanga umakhala kuti unamwalirapo
ngati? Umaphunzirira pomwepo kumwalira.
Kuphunzira sikutha.
- Pa moyo wa munthu pamakhala zambiri zoti uphunzire ndipo
umaphunzirabe mpaka kudzamwalira. Ena amati kumwalirako
ndi phunzironso palokha. Nanga umakhala kuti unamwalirapo
ngati? Umaphunzirira pomwepo kumwalira. Kungoti kumatha
ukakhala kuti wamwalira.
Kupsa n’kupsa thuza.
-Kawirikawiri zolakwa zazing’ono tikaziikira mang’ombe
zimaoneka zazikulu.
Kupulumukira m’kamwa mwa mbuzi.
-Kupulumuka pa mlandu chifukwa chonena bodza. Nkhani
yake imati, tsiku lina anyamata awiri anapeza mbuzi itaman-
gidwa pamtengo wina ndipo anaganiza zoti aibe. Atangoyamba
kumasula chingwe cha mbuziyo, mwini wake anabwera ndipo
anawafunsa kuti, “N’chifukwa chiyani mukumasula mbuzi
yanga?” Anthuwo anayamba kuchita mantha. Koma m’modzi
anati, “Tinaona kuti pano palibe msipu wabwino, ndiye
104