Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 104
Miyambi ya Patsokwe
Kupatsa n’kuyikiza.
-Ukamathandiza anzako, nthawi ina nawonso amadzakuthandi-
za.
Kupempha si kuba.
-Kuuza munthu kuti akuthandize si kulakwa.
Kupenya kumwamba n’kukhala ndi Nkhuku.
-Munthu ukakhala ndi chinthu umayesetsa kuchiteteza monga
munthu akakhala ndi Nkhuku amayesetsa kuziteteza kwa
Mphamba.
Kupenya pawiripawiri kudathyola khosi.
-Ndi bwino kusankha kuchita chinthu chimodzi m’malo mochita
zambirimbiri nthawi imodzi.
Kupepera kulibe mankhwala.
-N’zovuta kusintha kapena kuthandiza munthu wopepera.
Kupha Galu wachiwewe n’kulelemeza mpini.
-Pofuna kugwira munthu wochenjera kwambiri pamafunika ku-
mufatsira komanso kumutenga bwino.
Kupha mbalame ziwiri ndi mwala umodzi.
-Kupeza mwayi waukulu kwambiri mosayembekezereka.
Kupha Mkango ndi kuweteka.
-Pofuna kuchita zinthu pamafunika kufatsa ndi kupeza nzeru
yeniyeni.
Kupha n’kupha umakumbuka poguza.
-Tisanayambe kuchita chinthu tiziyamba tadzifunsa kuti, ‘Kodi
zimenezi zitha bwanji?’
Kupha Njoka n’kudula mutu.
-Kupha njoka kumafuna kuimenya mutu. Kuthetsa nkhani
n’kulinga utadziwa chimene chayambitsa. Kuti uthane ndi vuto
umafunika kuthana ndi chimene chikuyambitsa vutolo.
103