Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 103

Miyambi ya Patsokwe Kuonda saombezera. -Ngati takumana ndi mavuto, tisamathamangire kuloza ena zala. Kuonera patali, nyani anadzipha yekha. -Si bwino kumangotengera zinthu zomwe sukuzidziwa bwinob- wino kapena chifukwa c choona kuti ena zikuwayendera. Kuonerana m’kodi. -Mawuwa amatanthauza kunyozana, kudererana kapena ku- chitirana mwano. Kuonerana m’madzi. -Mawuwa amatanthauza kunyozana, kudererana kapena ku- chitirana mwano. Kuopa n’kukhala pambuyo ngati mchira. -Munthu amene akufuna kuchita bwino ayenera kuona mmene ena akuchitira. Kupata kumasiyana. -Anthu amapeza zinthu mosiyana, ena amapeza zambiri kuposa anzawo. Kupata n’kosiyana. -Anthu amapeza zinthu mosiyana, ena amapeza zambiri kuposa anzawo. Kupatsa n’kudzala, kunama n’kukazinga. -Ukathandiza mnzako umakhala ngati wadzala, mawa adzakuthandiza iweyo. Kupatsa n’kuika, kunama n’kukazinga. -Ukathandiza mnzako umakhala ngati wadzala, mawa adzakuthandiza iweyo. 102