Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 102
Miyambi ya Patsokwe
anthu.
Kunkira nsale n’kumodzi.
-Nsale ukamakula umakulira kofanana. Nafenso tizichita zinthu
mogwirizana komanso mofanana kwambiri ngati amodzi.
Kuno n’kunja kudayanja lichero.
-Ukalemera usamanyoze anzako, zamawa sizidziwika.
Kunong’oneza bondo.
-Mawuwa amatanthauza kudandaula utakumana ndi mavuto
chifukwa cha kusamva kapena kunyalanyaza machenjezo.
Kunyaza Katumbu n’kuvuula mono.
-Katumbu amakonda kuba msomba m’mono. Kuthana naye
n’kungovuula monowo. Chimodzimodzinso ndi ena omwe
amachita zinthu zosokoneza monga kuba, kuti uthane nawo
umafunika kumatseka chitseko chako ndi loko.
Kuolokera pakangaude.
-Kukhala ndi mwayi wopulumuka m’mavuto mosadziwika
bwino.
Kuombera mapira pamutu.
-Kuchenjerera mnzako pomubisira zoyenera kuchita kapena
kusamuuza zoona zenizeni.
Kuona chidameta Nkhanga mpala.
-Kukumana ndi mavuto kapena kukhaula.
Kuona Fisi si kubadwa kale.
-Mawuwa amatanthauza kuti ngakhale mwana akhoza kudziwa
zambiri kuposa munthu wamkulu.
Kuona maso a nkhono n’kudekha.
-Kudekha komanso kuugwira mtima kumathandiza kuti upeze
zabwino. Munthu wofatsa amadziwa komanso kuona zambiri
kuposa munthu wopupuluma.
101