Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 101

Miyambi ya Patsokwe Kumwamba ndi kumwamba, pansi ndi pansi. -Tiyenera kumanena zimene tikudziwa osati zongopeka. Kunama n’kudzipha. -Anthu samathandiza munthu wabodza akakhala pamavuto. Kunda adafa ndi diwa. -Kunda ndi mbewa yaikulu. Mbewayi imatha kufa ndi diwa ngakhale kuti ndi yaikulu. Kanthu konyozeka kangathe kupweteka ngakhale munthu wamkulu. Kunena kuti manda akufewa, n’kuika munthu ali m’maso. -Malangizo othandiza amachokera kwa munthu amene waona zambiri pamoyo wake. Kunena kwa ndithendithe Nanthambwe adadzitengera tsoka. -Munthu uyenera kumanena utaganiza bwinobwino, m’malo mongonena kuti nkhani ithe chifukwa zikhoza kukubweretsera mavuto. Kunena kwa ndithendithe Nanthambwe adazitengera. -Si bwino munthu kudzitama kapena kulonjezeratu chinthu zotsatira zake zisanadziwike kwenikweni chifukwa mwina zotsatira zake zitha kukuika m’mavuto kapena kukutsutsa. Si bwino kumafulumira kuyankhula kapena kuulura zinsinsi za ena chifukwa ukhoza kupalamula. Kunena ndi mtima umodzi. -Mawuwa amatanthauza kunena mosatsimikiza. Kungapande tambala kudzacha. -Ndi mawu amene anthu amadzilimbitsa nawo mtima akakhala paulendo. Amadziwa kuti ngakhale pangapite masiku, koma adzafika kawo. Kunja kuli kutali. -Munthu asamaderere dziko chifukwa dziko silitha, amatha ndi 100