Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 100
Miyambi ya Patsokwe
mnzeru kuti ena akadzamwalira zinthu zisadzaime. Mwambiwu
unachokera pa mawu omwe anthu ena ankanena akamafuna
kuti wina awafunire mankhwala. Ankangoti, “Mukatikumbire
mankhwala.” Anapitiriza kupemphabe mpaka munthuyo
anamwalira. Akanakhala anzeru akanafunsa munthuyo kuti
awauze mitengo yake kuti azikakumba okha.
Kumbuyo kulibe maso.
-Zimene zinachitika kale sitingazisinthe. Tiyenera kumaganizira
zam’tsogolo zomwe tingazisinthe.
Kumene kutalire n’kunsonga.
-Mawuwa amatanthauza kuti amene atagonje ndi wamng’ono.
Anthu akamamenyana, amene amayamba kulira ndi ana ndiye
anawo akuyerekezedwa ndi kunsonga. Mawuwa amanenedwa
pamasewera poderera ena kuti ndi ana.
Kumeneku n’kukonza chitseko chimera chitatha.
-Mawuwa amanenedwa poseka munthu wozengereza. Ena
amazengereza kupalira m’munda. Mbewu zawo zikayamba
kuwonongeka mpamene amayamba kupalira. Ena angamaone
kuti chimera chawo chikubeda, koma n’kumangonyalanyaza.
Akamaganiza zoti akonze chitseko chawo, amapeza kuti chime-
ra chija chatha.
Kumira pachipande.
-Mawu okokomeza omwe amatanthauza kuti munthuyo akuna-
ma mopanda manyazi.
Kumva mawu a akulu n’kuchezera.
-Mawuwa amatanthauza kuti, kuti munthu amve zimene aku-
luakulu akukambirana amafunika kukhala maso osagona. Ame-
ne akufuna zinthu zimuyendere ayenera kumvera zimene aku-
luakulu akumuuza chifukwa aona zambiri pamoyo wawo.
99