Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 10

Miyambi ya Patsokwe kuno zoti anthu amalodza anzawo kapena kuwachesula kuti akumane ndi zoopsa. Aliyense adzadya thukuta lake. -Munthu amafunika kulimbikira ntchito kuti apeze zimene aku- funa. Aliyense akondwa potsiriza. -Munthu amasangalala akamaliza kugwira ntchito mwakhama n’kulandira malipiro ake. Amadziombera ng’oma yekha. -Mawuwa amanena za munthu amene amakonda kuuza ena zo- khudza zimene amachita komanso luso lake. Amalume khalani pansi, ana akudziweni. -Si bwino kumangokhalira kuyendayenda. Ndi bwino kumakha- lako pakhomo nthawi zina. Amapatsa mosiyana. -Si bwino kusirira kapena kuchitira nsanje anzathu opeza bwino kapena amene zikuwayendera. Amene akufuna kuswa fupa amapita kuuzimba. -Ukafuna chinthu umafunika kugwira ntchito. Kuti uswe fupa la nyama umafunika kukasaka nyama kuthengo m’malo mongo- longedza miyendo n’kumadikira kuti ikupeze pamene wakhala- po. Amene amagona kunsi kwa mwala, ndi amene amaona mwala ukupuma. -Ngati munthu ukufuna kumva zoona za zinthu ungachite bwino kufunsa amene analipo pamene chinthucho chinkachi- tika. Amene umadya naye mbale imodzi ndi amene amakupereka. -Mnzako amene umamukhulupirira ndi amene amakupereka 9