Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 99
Matigari
Ndinatero. Koma iye anandiyankha kuti: ‘Ayi, sindikunena zim-
enezo. Ndikunena za anthu omenyera ufulu wawo omwe
anathawira kunkhalango. Abweransotu. Anthu olimba mitima
aja abweranso ndithu.’ ‘Mwandimanga m’masambatu pame-
nepo. Chachitika n’chiyani?’ Ndinamufunsa choncho. ‘Kodi un-
gakhulupirire? Ndi munthu wamfupi kwambiri. Ndati chiyani?
Ndi wamfupi. Ndi wamfupi ngati chitsa ndipo anavala chisoti
chozika nthenga komanso ananyamula chijasi chachikopa cha
kambuku paphewa pake. Koma kenako anangosintha n’ku-
sanduka chiphona. Ndikutitu chiphona! Anaima ngati Goliyati
n’kuuza wapolisi yemwe anali ndi galu kuti: ‘Ndine Matigari
ma Njiruungi, ndipo ndikukuchenjeza, musiye mtsikanayo
msanga!’ Kodi ndingafotokoze bwanji? Mawu ake anali ngati
chiphaliwali. Galu amafuna kuluma mtsikanayo anachita man-
tha n’kupsatira mchira wake. Kodi unayamba wamvako zangati
zimenezi?’ Pamene amandiuza zimenezi ndinangoona moto
ukuphulika kufakitale ndipo ndinadziwa kuti kwaipa. Ogwira
ntchito amawotcha ziboliboli za a Boy ndi a Williams zomwe zi-
nali panja pafakitaleyo. Ogwira ntchitowo anasangalala kwam-
biri kuona zibolibolizo zikunyeka ndi moto. Kenako ndinamva
mawu a Ngaruro wa Kiriro omwe anatengedwa ndi mphepo
pomwe amayankhula pa chinkuzamawu. Mundimvetsetsetu
pano, ndangogwira mawu ake omaliza. Anati: “Atsamunda
amenewa komanso antchito awo ayenera kulongedza katundu
wawo azipita kwawo. Anthu okonda dziko lawo, a Matigari ma
Njiruungi, abweranso ndipo ogwira ntchito ayenera kugwiri-
zana ndi Matigari. Wodzala ayenera kukolola mbewu zake! Ife
takana kukhala ngati mapoto omwe amaphika koma osadya na-
wo!”
98