Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 97
Matigari
“Anzanganu munandifunsa funso, koma sindinaliyankhe.
Mwachidule ndinene kuti: Ndapezeka kuno chifukwa malinga
ndi zimene akunena, akuti ndilibe chikalata chosonyeza kuti
nyumbayo ndi yanga. Koma tandiuzeni, kodi munthu angafu-
nenso chikalata chamtundu wanji kuposa thukuta komanso
magazi omwe ndinakhetsa kungochokera pamene tinayamba
kuyedzeka maziko a nyumbayo mpaka khoma kumakwera? Ko-
di tilowere kuti ife anthu omenyera ufulu wa dziko lathu, ife a
Matigari ma Njiruungi?”
“Matigari ma Njiruungi?” anthu awiri omwe anali asa-
nayankhule aja anakuwa nthawi imodzi. “Kodi ndinu amene
chakumasanaku munalanditsa mtsikana kuchokera m’kamwa
mwa galu wolusa uja?”
Anthu ena onse aja anadabwa kwambiri atamva zimene an-
thuwa ananena.
“Kodi ndinu munthu amene Ngaruro wa Kiriro amanena
kufakitale kuja apolisi asanabwere n’kuyamba kuthyola dzipala-
pasiro za ogwira ntchito?” m’modzi mwa anthu anayankhulira
limodzi uja anafunsa.
“Apolisi asanabwere n’kuyamba kuthyola dzipalapasiro za
ogwira ntchito? Liti? Lero?” ena omwe anali museloyo anafunsa
akuyang’ana munthu yemwe ananena zimenezi uja.
“Kodi simunamve mmene apolisi atibulira anthu kufakitale
lero?”
“Nanunso tatiuzani chimene chachitika kuti mupezeke
kuno.”
“Onse anakhala tsonga n’kuimika makutu akuyang’ana
munthu ankayankhula uja pamene ankayamba kufutukula
nkhani yake.”
96