Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 96
Matigari
“Kenako ndinatopa nazo moti ndinayamba kulimbana ndi
Mtsamundayu chifukwa cha zimenezi.”
“Ndinalumbira kuti ndidzamenyera nkhondo ufulu wanga
komanso wadziko langa mpaka nditamupirikitsa. Tsiku lina
ndinapita kwa Mtsamunda Williams n’kumuuza kuti alongodze
katundu wake n’kutuluka m’nyumba yanga ndipo ndinamu-
lozera nsana wanjira yakwawo. Ndinamuuza kuti, ‘Pita
ukamange yako nyumba. Nawenso manja uli nawo ako.’ Koma
anagwira chiputu. Sankafuna kutuluka. Kenako anathamangira
kumene kunali lamya ndipo ine ndinathamangira kumene
kunali mfuti. Koma kodi mukumudziwa amene anandulumphi-
ra akukuwa kuchenjeza Mtsamunda Williams? Analitu John
Boy! Nditalimbana naye, ndinamupulumuka m’manja n’kutha-
wa kudzera pazenera kupita kumapiri. Mtsamunda Williams
ndi John Boy anayamba kundisakasaka. Tinalimbana kwa zaka
zambiri ndipo tinkangokhalira kusakanasakana paliponse. Ndi-
nayamba ndi kuzimitsa John Boy. Ndipo dzulodzuloli ndathana
ndi Mtsamunda Williams. Ndinamuonetsa zoopsa moti kenako
ndinamuponda pachifuwa nditakweza zida m’mwamba
kutsimikizira kuti ndamulumitsa mano. Popeza ndinali ndita-
pambana nkhondo, ndinaganiza zobwerera kwathu kuti ndi-
katenge nyumba yanga.”
“Abale anga! Simungakhulupirire malodza amene ndinaona
nditafika kunyumba yanga ija! Mukuganiza kuti ndi ndani ame-
ne ndinamupeza ataima pageti la nyumba yanga? Mwana wa
John Boy komanso wa Mtsamunda Williams! Pamenepo
mpamene ndinazindikira kuti mwana wa Boy ndi amene
anatenga makiyi a nyumba yanga. Kenako anakoka chingwe
kupolisi moti posakhalitsa apolisiwo anatulukira n’kundigwira.
Kodi chilungamo chili kuti m’dziko lino makosana?”
95