Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 94
Matigari
akuwerenga Baibulo pagome.
"Ndiyeno nthawi ya chakudya chamadzulo itafika, anakhala
pagome limodzi ndi ophunzira ake. Iye anawauza kuti: Ndi-
nalakalaka ndithu kudya chakudya chimenechi pamodzi ndi
inu, pakuti ndinena ndi inu, sitidzadyanso limodzi chonchi ku-
fikira Ufumu ukadzabwera. Ndipo mmene adatenga mkate, na-
yamika, anaunyema, anawapatsa n’kuwauza kuti: Ili ndi thupi
langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro
changa kufikira ndidzabwerenso kachiwiri. Kenako anatenga
chikho, ndipo pamene anayamika, anati, chikho ichi ndi pan-
gano latsopano la pakati pathu chifukwa cha magazi athu. Muzi-
chitirana zimenezi kufikira ufumu udzabwere, mogwirizana ndi
chifuniro chanu.”
Wamowa uja anasiya kuyankhula. Kenako anatembenukira
kwa Matigari:
“Tatiuzeni zoona. Kodi inuyo ndi ndani? Chifukwatu sindi-
naonepo munthu atalowa m’ndende ndi chakudya kapena
mowa. Ndamangidwapo nthawi zosawerengeka, koma ndiku-
lumbira makate Baibulo, sizinayambepo zachitika kuti anthu ku-
mangidwa osasechedwa mokwanira akamalowa muno . . .
Nsapato zathu, ndalama komanso zina zonse zimatsala panja.
Ndiye lerolo chachitika n’chiyani? Ayi ndithu, kamba anga
mwala! Tatifotokozereni bwinobwino chimene chachitika!”
Kenako anakhala pansi. Anthu onse anali muselo muja
anatembenukira kwa Matigari, ndipo ankayembekezera kuti
awauza chinachake chapadera, chifukwa zimene wamowa uja
ananena zinali zoona ndithu. Onse anamangidwa patsikulo. Ko-
ma palibe amene analandidwa zinthu zake. Ndiyeno Matigari
anayamba kuyankhula ngati mmene bambo amayankhulira kwa
ana ake.
93