Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 93
Matigari
“Limenelo silingakhale vuto, ndikhoza kudya zimene
mungasiyezo,” anatero wakuba nsima uja.
“Chifukwa chiyani? Kodi nawenso ndi woipa mtima
mofanana ndi bambo wa munkhani ija, yemwe anapanirira yek-
ha poto wa chakudya mkazi wake woyembekezera akufa ndi
njala?” woyendayenda uja anafunsa. “Kapena uli ngati anthu
oipa mtima omwe akuyendetsa dziko lino?
Ndi mlimi uja yemwe anali ndi yankho la vuto lawoli.
“Ndinamangidwa pamene ndimachokera kogula makandu-
lo,” anatero. “Tikhoza kuyatsa m'modzi kapena muwiri kuti
azitiunikira tikamadya. Ndi njalayidi wina akhoza kupezeka wa-
tafunira limodzi ndi chala cha mnzake. Nanga mdima wake
umenewu nthuni? Koma vuto ndi lakuti ndilibe machesi.”
“Ine ndili nawo,” anatero mphunzitsi uja.
Anayatsa makandulo awiri. Kenako anayamba kuyang'anana
nkhope ngati akufufuza munthu amene anawapatsa
chakudyacho. Pankangooneka zithunzithunzi ndipo zina zinka-
onekera pakhoma. Kenako anayamba kuyang'ana Matigari
mwachidwi.”
Matigari anatenga chakudyacho n'kuchinyemanyema ndipo
kenako anawapatsa. Anthuwo anayamba kudya. Kenako
anatenga botolo la mowa lija, kulitsegula ndi mano ndipo ke-
nako anapungula pang'ono pansi ngati nsembe yoteta mizimu
yamakolo. Kenako anapereka botololo kuti aliyense akonkheko
kukhosi n’kupereka kwa mnzake.
Ndiyeno litafika pa woledzera uja, anaimirira atagwira
chakudya chija ndi dzanja limodzi komanso botolo la mowalo
ndi dzanja linali ndipo anayamba kuyankhula ngati
92