Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 91

Matigari anali asanafotokoze chifukwa chimene anamangidwira. “Kodi ndi zoona kuti mtsogoleri wadziko lino ndi wopanda chifundo?” mlimi uja anawonjezera motero. “Nkhwani sawot- chera, jekete sapisira! Kumena mosapsatira, sikuti ndikunena izi chifukwa cha kaduka kapena kudana ndi olamulira athu. Enafe tamangidwa popanda chifukwa. Komanso atilakwira kwambiri potitsekera muselo yopanda ndi chimbudzi chomwe ngati ino. Mapeto ake tikungokodzerana komanso kupakana matudzi!” “Ngakhale zimbudzizo zikanakhalako,” uja ankaimbidwa mlandu wakuba nsima anawonjezera,“bwenzi tikupita ku- chimbudziko kuti tikadonthezereko chiyani kumimba kuli pulu- lu? Ndachita kuiwaliratu tsiku limene ndinaponyeramo kanthu m'mimbamu! “Ingolekani musakambe.” anatero anagwidwa akufuna kuba kachikwama kandalama uja, “Njala si mmene ikundisweramo!” “Ndakhala ndikuwerenga m'manyuzipepala kuti kundende amapereka chakudya chaulere,” mwana wakukoleji uja anatero. “Inde, komatu amadya Mulungu akalola! Woledzera uja anatero mokweza. Pa nthawi imeneyi mpamene Matigari anakumbukira kuti anali adakali ndi zakudya zija komanso botolo la mowa. “Ndili ndi tizakudya tomwe ena anandimangira mpepala chakumasanaku. Ndilinso ndi botolo la mowa. Tiyeni tonse tiga- wane chakudyachi komanso timweko pang'onopang'ono mowa- wu. Zimenezi zithandiza kuti maso ayere komanso kuti ma- tumbo athu asanyenyeke ndi njala. Si kuchuluka kwa chakudya komwe kuli kofunika, koma kugawana kangachepe kamene ka- pezeka. Kale tinkaimba kuti: 90