Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 9

Matigari tsopano ndipo magazi awo akangosakanikirana ndi dothi, ankakhala asilikali okonzeka kumenya nkhondo yolimbana ndi atsamunda.* *Zimene zafotokozedwazi zinkachitika pachinamwali pomwe anthu ankaimba nyimbo komanso kuvina mwambo wa mdulidwe ukamachitika. Zimenezi zingaimirenso zimene anthu anakumana nazo nkhondo yolimbana ndi atsamunda isanachitike. Maganizowa atamuchoka, anaimirira n'kuyang'ana kumene anakwirira zida zake kuja, ndipo anayamba kudziyankhulira yekha mong’ung’udza kuti, “Zili bwino tsopano kuti ndakwirira zida zanga.” Ndiyeno anadula khungwa lamtengo wina n'kulimanga m'chiuno mwake. Kenako anang’ung’udzanso kuti, “Ndadzimanga ndi lamba wamtendere. Tsopano ndipite kwathu kuti ndikamangenso nyumba yanga.” Kenako anawoloka mtsinje uja n’kutuluka m’nkhalango. 8