Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 89
Matigari
Wina anamangidwa pamlandu wopha mpondamakwacha
wina chifukwa ankalephera kumulipira ndalama yaganyu yo-
lima yomwe anagwira.
”Amangondipondetsa moti ndinafika potopa nazo. Ko-
mansotu ndinangomumenya ndi ndodo basi, kenako anagwera
pansi n'kumwalira . . . zimene amachita zinandikwana.
Tangoganizani kunyumba mkazi komanso ana akudikirira kuti
upititse ya ufa, koma iwe n'kupitako chimanjamanja. Ndipotu
sikuti ndinapita kukapempha. Ndimakatenga ndalama zomwe
ndinakhetsera thukuta langa.”
Wina anamangidwa chifuka ankangoyendayenda m'tauni.
“Kodi anandipatsapo mwayi wantchito? Amangolembana
pachibale basi. Tangoganizani kumangidwa chifukwa chopeze-
ka ukuyendayenda m'dziko lako lomwe.”
Pagululi panalinso wophunzira kusukulu yaukachenjede
yemwe anauza mkulu wina waboma kuti zinthu sizikuyenda
bwino kungochokera pamene dziko lawo linalandira ufulu
wodzilamulira.
“Kodi mukudziwa zimene ndinamufunsa? ‘N’chifukwa chi-
yani mumavalabe mayunifomu omwe atsamunda ankavala?’
Nanga iwowo ndi milungu kuti tisamawafunse mafunso? Ko d i
demokalase ili kuti m'dziko muno? Mkulu wabomayo anaopseza kuti:
‘Muona zokhoma ana a kuyunivesite inu!’ Atanena zimenezi
ndiye ndinamumasura. Ndinamuuza kuti, ‘Inuyo, mwalephera
kukwaniritsa udindo wanu, nanga chikuchitika n'chiyani
m'dzikoli? Kodi nanunso ndi zidole za akuluakulu a boma?’ At-
amva zimenezo anakwiya nane n’kunena kuti, ‘Taonani ana
osapola panchombo akutukwana anthu akuluakulu!’ Koma ine
ndinamuuza kuti kukula si kanthu. Kuona fisi si kubadwa kale.
88