Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 87

Matigari “N'chifukwa chiyani ukutinyowetsa ndi mkodzo wakowu? Zoona ungamakodzenso mmene tathinikiziranamu!” “Ukungokhaliranso kutsitsa mpweya apa, m'mimba mwakomo muli bwinobwino koma?” “Ndani, ineyo?” woledzerayo anafunsa tulo tili m'maso ko- manso akuoneka kuti mowa ukadamulamulira. ”Ndikuthandiza kuti mvula igwe.” “Kuphwisa, kusanza ndi kukodzako?” wina anafunsa. “Ndikulumbira pali nthumbira ya agogo anga kumanda, inetu ndikungothandiza kuti mvula igwe! Simukuona pamene chilala chafikapa? Tangogwirani makomawa mumve mmene akutenthera. Ndisanamangidwe, ndinaima m'mbali mwa nsewu. Chomwe ndimaona ndi udzu wouma komanso masam- ba ouma kakata! Kenako ndinadzifunsa kuti: ‘Ngati nditathan- dizako kugwetsa dontho limodzi kapena atatu padzikoli, Namalenga akhoza kuona zimenezo n'kutikomera mtima. Akhoza kutigwetserako misozi yake yomwe ingathandize kuti dzikoli litsitsimuke, ndipo zimenezi zingapindulitse tonse.” “Ndiye tinganene kuti masanzi akowo ndi nsembe yopita kwa Chisumphi?” winanso anatero mwachipongwe. “Ndiye kuti chiphwisi chako chija chinali chiphaliwali?” winanso anatetemula motero. “Mvula, mvula bwera lero, kuti ndikuphere mwana wang'ombe. Komanso wina walinunda pamsanapa!” winanso anaimba motero. Ena ankangoseka. Koma ambiri ankaonekabe okwiya ndipo zinkaoneka kuti phokoso linkachitikalo linkawakanda padazi. Kenako angapo anayamba kutsirira ndemanga pa zimene woledzerayo ananena. 86