Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 84

Matigari Bwarani anthu anga, nonse, tiyeni tilowe m'nyumba yathu chifu- kwa mtima wanga ulibe nsanje komanso sine wodzikonda ngati enawa!” Matigari ananena mawu amenewa ngati akuuza khamu la anthu. “Inde, bwerani nonse, tiyeni tiyatse moto m'nyumba yathu limodzi! Tiyeni tidyere limodzi chakudya, komanso tiimbe mosangalala ndi mtima umodzi!” Pamene ankati aziyamba kutsegula geti ija, Matigari anamva kulira kwa galimoto. Kenako anangoona mwadumpha anthu atanyamula matochi. Inali Land-Rover ndipo inangoti kwii n’kuima pamene anali paja. Amene anadumpha aja anali apolisi ndipo m'modzi anatsala kumbuyo kwa galimotoyo atagwira ga- lu. “Wapi ule mwivi?”* m'modzi wa apolisiwo anafunsa. *Wapi ule mwivi (Kiswahili): kutanthauza “kodi wakubayo ali kuti?” Robert Williams anatulukira atakwera hatchi. Williams yemwe anali mzungu ndi Boy yemwe anali wakuda, onse pamodzi analoza Matigari. Apolisiwo anagwira Matigari n'ku- muunika ndi tochi kumaso. “Ni ule mzee! Ni ule mzee!” m'modzi wa apolisiwo anatero.* Ni ule mzee (Kiswahili): “Ndi bambo tinakumana naye uja.” Apolisiwa anali omwe aja Matigari anakumana nawo masa- na. “Kodi bambo inu ndi amisala eti?” anafunsa wapolisi m'modzi yemwe masana uja ankafuna kulumitsa Guthera galu. Kenako anamunyamula n'kukamuponyera mu Land-Rover ija ngati chipika. Atagwera m’galimotomo galu anagwidwa uja anayamba kulira moopseza kwinaku akumukukuta mano. “Tionanatu kuphwando,” John Boy ndi Robert Williams anatsanzikana motero pamene ankasiyana. 83