Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 83
Matigari
zinthu zonse za munthu.
"Kodi ameneyu si mwana ankalephera kumina yekha uja?
Ndi ndani anamupatsa udindo woti agulitse malo athu,
mafakitale, nyumba komanso cholowa chathu? Kodi anthu inu
munakumana kuti? Ifetu tinkaganiza kuti anthu ophunziranu
muima nji polimbana ndi atsamunda omwe amakolola pamene
sanalime. Kodi ku Ulaya unapita kuja unkakangosewerako eti?
Unayamba bwanji kucheza ndi anthu a mtundu umenewu, om-
we amangokhala ngati nthata zoyamwa ena magazi?"
Robert Williams ndi John Boy anayamba kunong'onezana.
Kenako Williams anamenya hatchi yake n'kunyamuka kumapi-
ta. Matigari anayamba kutsegula geti lolowera kunyumba ija.
"Tadikirani kaye madala! Popeza mwanena kuti mulibe
chikalata chosonyeza kuti nyumbayi ndi yanu, ndiye mwadziwa
bwanji kuti ndiyanudi?" anatero John boy.
Ankayankhula monyoza zedi, koma Matigari sanamulabade.
Chikhumbokhumbo cholowa m'nyumbayo chinali chitamug-
wira ndipo chinamukumbutsa zimene zinachitika kale pamene
anayamba kulimbana ndi Mtsamunda Williams. Anakumbukira
mifuleni yathukuta lomwe anakhetsa, kutopa, mvula, mphepo
yomwe inamuumbudza, ululu komanso mavuto onse omwe
anakumana nawo.
“Tabwera kuno!” anatero Matigari akuyang'ana John Boy
m'zikope mwenimweni. Matigari anali ndi khalidwe lapadera.
Iye anali ndi mawu aukumu omwe ankachititsa kuti anthu
azikopeka naye akamayankhula. Tsopano Matigari ndi John Boy
anaima maso ndi maso ngati akupimana mphamvu kuti aone
amene ali wanzeru kwambiri. “Tiye kunyumba yanga ndi-
kakuonetse makona onse a nyumba imeneyi, komanso ndi-
kakuonetse zipinda zonse zomwe ndinazivutikira kuzimanga.
82