Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 82

Matigari "Zoonadi," anatero Robert Williams. "Ndikufunanso nditamva kuti nkhani ya sitiraka ija yatha bwanji. Muuze mdalayo kuti anya- muke azipita madzi asanachite katondo. Akachita masewera . . . Ha-ha -ha-ha! N'chifukwa chiyani sunamufunse kuti akuonetse chikalata chosonyeza kuti nyumbayi ndi yake? Nyumba yake! Ha-ha-ha-ha!" "Muli ndi chikalata chosonyeza kuti nyumbayi ndi yanu?" "Manja angawa ndiye chikalata chenicheni chosonyeza kuti nyumbayi ndi yanga. Kodi mukufunanso chikalata chamtundu wanji kuposa magazi omwe ndinakhetsa pomanga nyumbayi?" "Tsopano ndikupatseni malangizo madala. Nyumbayi ndi yanga. Nyumbayi komanso mindayi ndi zanga. Ndinagula zin- thu zimenezi kuchokera kwa mwana wa Howard Williams. In- de, ndikutanthauza malo onse mukuwaonawa." "Wati Howard Williams?" "Inde. Ndi mwana woyamba wa a Williams. Ndi munthu wofunika kwambiri. Ndiye samala chifukwa si munthu wamba. Kunyoza munthu ameneyu n’chimodzimodzi kugenda kupolisi chamba chili m’thumba. Ndi mkulu wa Anglo -American Interna- tional Conglomerate of Insurance (AICI) komanso wa Agribusiness Co -ordinating International Organisation (ACIO); komanso ndi mtsogo- leri wa bungwe losunga ndalama la Bank ers' Internatio nal Un- ion (BIU)* Ineyo komanso iyeyu ndi mamembala akuluakulu a komiti yoyang'anira kampani ya Leather and Plastic Facto ry. Nduna ya Zachilungamo ibwera kudzakumana nafe mawa. Munda wa tiyi ukuuona tsidya lina lamsewulo ndi wa Robert Williams. Wamvetsa tsopano mdala? Kodi wamvetsa kuti munthu ndili nayeyu ndi ndani? Ndi mboni yanga chifukwa ndi amene anan- digulitsa nyumbayi." *Mawu ali m'mikutira mawuwo ali ndi matanthauzo m'Chigikuyu: Aici: akuba; Acio: Awo; Biu: kutengeratu zonse, kutanthauza 'akuba omwe amamukolopola 81