Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 81
Matigari
nyemba imodzi imene yagwera pansi."
"Zodabwitsa sizidzatha padzikoli! Kodi waiwala zimene an-
thu anachita posonkherana ndalama kuti akutumize kusukulu?
Kapena bambo ako sanakuuze zimenezi? Kodi anthu
ophunziranu simukumbukira kuti munaphunzira chifukwa cha
anthu omwe mukuwanena kuti zitsiru lerowa? Lero
mwasukusula n’kuyamba kuluma dzanja limene linakuthandi-
zani! Anthu alibedi pabwino, pabwino anatayira galu."
"Kodi munasainirana pati ndi bambo anga kuti ndikubwe-
zereni tindalama tomwe mukuti munanditumizira kusukuluto?
Ndionetseni kuti ndikubwezereni pompanopompano!" John
Boy Junior anayankhula mokuwa ngati kuti akuyankhula pam-
sonkhano wandale. "Ndionetsenitu pamene munalemberana!
Ndikubwezerani tindalama tanuto, komanso ndiwonjezerepo
chiwongoladzanja . . ! Tadikirani ndikuuzeni bambo, zimene
zili zanga, ndi zanga. Ngati mukufuna kuti nditenge zinthu
zomwe ndi zanu, shauri yanu! Pitani mukatenge zonse mun-
dipatse. Ndidzalandira zonse. Mwinanso mungachite bwino
kungonyamuka n’kumapita kwanu, ndisanakuonetseni
malodza. Kunjaku kwada kale, posachedwapa kunja kukhala
kuli chimdima. Sewero lathera pamenepa. Nyamukani
mwaulemu muzipita. Panopa nyumbayi ndi ya anthu ena, si ya-
nunso bambo, mwamva!"
"Wati ndi ya munthu wina? Ikhala bwanji ya wina ngati
anamanga ndi iyeyo? Ineyo ndi amene ndinamanga nyumbayi
ndipo sindichoka pano."
"Mdalayu ndi wamakani ngati wofula agalu. Eti akukakamira
kuti nyumbayi ndi yake," wakuda uja anauza Robert Williams.
"Tsopano ndithetse malonda amphakawa chifukwa mapeto ake
tichedwa kuphwando lokonzekera kubwera kwa nduna ija mawa."
80