Matigari
"Mwana iwe ndi wotembereredwa. Zoona ungakweze
mkono wako n'kumenya bambo ako?" Matigari anatero, atagwir-
abe geti ija.
"Inu si bambo anga! Tandiyang'anani bwinobwino kunja
kukadawala. N’kutheka kuti mukufunika mandala. Ine ndi John
Boy Junior. Wolemekezeka a Boy, omwe inu mukuwanyozawa
ndi amene anali bambo anga. Bambo anga anali munthu
wofunika kwambiri. Anali anzeru, otsogola komanso oona pata-
li. Iwo ananditumiza kusukulu pa nthawi imene anthu a m'dziko
muno sankaona kufunika kwa maphunziro. Ananditumiza ku
Fort Hare ku South Africa kudzera pasitima ya panyanja. Ke-
nako ndinapita ku England komwe ndinakaphunzira pasukulu
yaukachenjede ya Lo nd o n Scho o l o f Eco no m ics, yomwe ima-
konda kudziwika kuti LSE. Kumeneko ndi kumene ndinakanola
luso langa ndiponso kupeza masamba osiyanasiyana a sukulu
yanga monga madipuloma a adimisitireshoni. Ndili kumeneko
ndinkadya m'malo otchuka komanso odula kwambiri, komwe
ndinaphunzira kumavala modzilemekeza. Ndinaphunziranso
kusangalala ndi moyo kumabala otchuka. Koma nditangotsala
pang'ono kubwera kuno kuti ndidzawaonetse bambo anga
madigiri komanso masatifiketi anga, ndinalandira kalata yondi-
dziwitsa kuti bambo anga anapita kunkhalango ndi Major How-
ard Williams, kuti akathane ndi zigawenga. Zimenezo . . ."
"Tapumula kaye . . . ima pomwepo!" Matigari anamudula pa-
kamwa kwinaku akunjenjemera ndi chisangalalo. "Kodi ndiwe
mwana uja tinamutumiza kunja? Mwana uja ndalama
zamaphunziro ake tinachita kusonkherana, tikumaimba monya-
da kuti: Uyu nd iye m wana wathuwathu o sati wa m unthu w o b-
wera! Akadzabwerako adzamange mizinda m’dziko lathuli komanso
adzativuule muukapolo! Zoona ndiwe mwana yemwe
78