Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 75

Matigari akanamva. Iye sankayankhula modzikuza, koma ankayankhula mwaulemu komanso mokoma mtima monga mmene amachitira munthu yemwe akucheza ndi mwana. “Mwana wanga, kodi wandifunsa kuti zikutheka bwanji kuti nyumbayi ikhale yanga? Nkhani yake ndi yaitali . . . Pali zambiri zomwe ndingakuuze . . . Waiona nyumbayi? Waona minda ya tiyiyi komanso msewuwu? Kodi ukuganiza kuti amene anapan- ga zimenezi ndi ndani? Ndipo undimvetse, sikuti ntchito zime- nezi ndayamba kuzichita dzulodzuloli ayi. Ndakhala ndikugwira ntchito imeneyi kuyambira kale kwambiri iweyo usanabadwe. Tangoganiza, ndinalipo m’nthawi ya apwitikizi, m’nthawi ya aluya, komanso m’nthawi ya azungu—.” “Madala, sindikufuna kuti mundiphunzitse Histo ry*! Ndakufunsani za nyumbayi, ndiye ingoyankhani funso.” *History ndi phunziro lokhudza mbiri yakale. “Nyumbayi? Ukuganiza kuti mbiri ya nyumbayi ndi yo- siyana ndi zimene ndikufotokozazi? Manja ndi amene amapan- ga mbiri ya anthu. Kodi ukumudziwa Mtsamunda Williams, mzungu uja ankakhala m’nyumba imeneyi?” “Bob, m’kuluyutu akunena kuti bambo ako akuwadziwa!” “Bambo anga? Bambo angatu anasowa atapita kunkhalango zaka zapitazo. Kaya chinawachitikira n’chiyani, anangopezeka atafa.” “Inde, anafera limodzi ndi bambo anga. Nanenso ndakumbukira.” “Tamufunse kuti chinawachitikira n’chiyani. Sewero mukupangali likundiwaza kwabasi, mwinanso kuposa kukwera mahatchi.” Munthu wakuda uja anatembenukiranso kwa Matigari n’ku- mufunsa kuti: “Wati a Williams? Howard Williams? Mzungu uja ankakhala kuno?” 74