Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 74
Matigari
kunali nyumba ija ndi dzanja limodzi.
“Ndi munthu wabwinobwino kapena wopenga?” mnzungu uja
anafunsa mnzake wakuda uja. “Muchezetseniko pang’ono mnzanu,
eh? Mukhozanso kupanga kasewero, mukhoza kuchita chisudzo. Ineyo
ndikhala woonerera, awirinu mukhala akatswiri a zisudzo.”
“Nkhani ya zisudzoyitu ine ndiye si kwenikweni,” munthu waku-
da uja anatero. “Ndipo ngati nditachita, ndingakonde kupanga mbali
yomvetsa chisoni. Koma kuti ndikusangalatse, ndiyesetsa . . . Dzina
lako ndi ndani?” anamufunsa Matigari.
“Matigari ma Njiruungi.”
“Matigari ma Njiruungi?”
“Inde, mwabooleza.”
“Ndiye ukufuna chiyani kuno?”
“Ndikufuna makiyi a nyumba yanga.”
“Ukudziwa kuti nyumbayi ndi ya ndani?”
“Inde ndikudziwa! Ndi yanga. Nyumba imeneyi ndi ya ineyo
komanso banja langa.”
“Bob, akutitu nyumbayi ndi yake komanso ya banja lake . . . Zathe-
ka bwanji kuti nyumbayi ikhale yako?” iye ankayankhula ndi
Matigari modzipopa kwambiri ngati mmene amachitira wapolisi
akamafunsa mafunso munthu woledzera.
Funso lakuti, “Zatheka bwanji kuti nyumbayi ikhale yako?”
linadzutsa mbozi ya khalee m’mutu mwa Matigari, ndipo ana-
kumbukira zomwe zinachitika m’mbuyomo. Anapuma mousa
moyo. Kenako anasiya geti lija n’kutembenukira munthu waku-
da uja. Ndiyeno anayamba kuyankhula naye. Tsopano zinkango-
khala ngati Matigari akufotokoza zinthu zozama kwambiri kwa
mwana wamng’ono, m’chinenero chimene ndi ana okha
73