Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 72
Matigari
Gawo 12
Mzungu komanso munthu wakuda anali atakwera pamsana
pamahatchi aja ndipo anali ataima m’mbali mwa msewu
waphula womwe unkalowa kugeti lina. Mahatchi omwe
anakwerawo ankaoneka mofanana. Onse ankaoneka ofiirirako.
Nayenso mzungu komanso munthu wakudayo anali atavala
zovala zofanana. Chimene chinkawasiyanitsa unali mtundu
wakhungu lawo basi. Koma tikakamba za mmene anakhalira pa-
mahatchiwo komanso mmene ananyamulira zikwapu ndiponso
zingwe zoyendetsera mahatchiwo, panalibe kusiyana. Komanso
mmene ankatafunira chingerezi, panalibe kusiyana kulikonse.
Zinkaoneka kuti anali akufuna kuti azisiyana.
“Bwanawe, tionana kuphwando madzulo ano.”
Ndiyeno ali mkati motsanzikana, anaona Matigari akuyenda
molunjika pamene anaimapo. Kenako anaimitsa mahatchi awo
n’kudikirira kuti aone kuti munthuyo akufuna chiyani.
Guthera ndi Muriuki anali ataima penapake kuseri kwa zi-
yangoyango zina ndipo ankangodikira kuti aone zomwe zitachi-
tike. Onse ankadzifunsa kuti: ‘Koma mutu wa munthu ameneyu
umakoka, kapena mawaya ena anaduka? Si nyumba zimenezi
zinali za atsamunda omwe anali m’dziko muno ndipo panopa
ndi za anthu ena olemera kwambiri, monga anthu ochokera
m’mayiko ena komanso ena a konkuno a mitundu yosiyana-
siyana—akuda, makaladi komanso azungu? Komatu Matigari
ankachita zinthu mosatekeseka komanso mosakayika
mpang’ono pomwe. Ndipo zimene ankachita zinkaoneka kuti
akudziwa chimene akuchita. Iye anayenda n’kudutsa anthu
anali pamahatchi aja ndipo anakafika pageti.
71