Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 71

Matigari “Nyumba ija . . . Nyumba ija ndi iyoo . . !” iye anakuwa mot- ero, mawu ake akunjenjemera ngati kuti akuchita zimenezi chifukwa chakunjenjemera kwa thupi lake lija. “Kuti?” Guthera ndi Muriuki anafunsa nthawi imodzi ngati anachita kugwirizana. “Iyoo, pamwamba paphiripo!” Guthera ndi Muriuki anaponya maso awo n’kuyang’ana kuphiriko ndipo anaona chinyumba chachikulu chomwe chinka- oneka kuti chadzadza phiri lonselo. Nyumbayo nayonso inkangooneka ngati munda watiyi uja chifukwa inkakhala ngati ilibe malire. “Nyumba imeneyoyodi ndi yanu?” Guthera anafunsa mo- sonyeza kukayikira. “Inde . . . ndi yanga! Nyumba imeneyo ndi imene ndakhala ndikumenyanirana ndi Mtsamunda Williams kwa zaka zambiri kufikira dzulo pamene ndinamulawitsa chipolopolo n’kuponda pachifukwa chake. N’chifukwa chiyani ndinalephera kuz- indikira munda watiyiwu, kulephera kudzindikira zinthu zanga zomwe! Tsopano tiyeni kunyumba kwathu . . . ” Anatero Matig- ari. Maso ake ankawala ngati nthanda. Tsinya lija linali litabalali- ka, ndipo anayamba kuonekanso ngati kamnyamata kabiriwiri. 70