Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 70
Matigari
tsiku lina ndikanadzauluka pamwamba pa tiyiyu nditakwera
Mercedez-Benz ya mapiko, kapena hatchi yamapiko. Ndikanad-
zaitsitsa m’munsi pang’ono kuti masamba a tiyiyu azichotsa
fumbi la kumapazi anga . . .” Muriuki anagwiritsa ntchito mwa-
yi wa maloto aulele, omwe munthu sumafuna kumawalota
mosinira.
Koma malodza sadzasiya kuchitika padzikoli. Kaya chinali
chidima chomwe chinabwera chifukwa cha kutentha kwa dzuwa
lomwe linkawawomba kumasolo, kaya kunali kutopa, onse ata-
tu anadabwa ndi zimene anaona. Anaona gulu la mahatchi liku-
thamanga kulowera chakumadzulo ndipo m’mbuyo mwawomo
anangosiya fumbi lili kobo. Fumbilo linkangokhala ngati liku-
landiridwa ndi dzuwa lakachisisira lomwe linkaomba madzu-
lowo.
“Taonani, kutsogoloko! Kodi si mahatchi amenewo?” Guthe-
ra anafunsa modabwa.
Iwo anayamba kutsatira mapazi a mahatchi aja, ngakhale
kuti zinali zovutanso kuona mapaziwo bwinobwino. Mahatchi
aja anapitirizabe kuthamanga kulowera chakumadzulo. Kenako
mtambo wofiira unaphimba dzuwa lija, koma linkakhalabe ngati
likusuzumira m’mitambomo n’kumaoneka ngati mapaipi omwe
anamwazikana kulowera mbali zosiyanasiyana.
Posakhalitsa anazindikira kuti silinali gulu la mahatchi.
Anali mahatchi awiri okha basi. Koma sikuti ankawaona
bwinobwino kungoti ankamva kulira kwa mapazi a mahatchiwo
ndipo anapitirizabe kuwalondola. Kenako Matigari anaima
mwadzidzidzi n’kuyamba kuloza kuphiri lomwe linali kutsogo-
lo kwake. Thupi lake lonse linkangonjenjemera ndi chisangalalo.
69