Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 7

Matigari Mtsamunda Williams anali atatsikira kuli chete, ndipo sankakayikira mpang’ono pomwe zoti walandilidwa ndi manja awiri ku Gahena monga malipiro a kuipa mtima kwake. Tsopano dzuwa n’kuti likuthamangira paliwombo, komabe kunja kunali ngululu moti sankatha kuona patali. Iye anali wamtali komanso wojintcha ndipo ngakhale kuti mavuto a ukalamba anali asanamunjate, ankaoneka wachikulire ndithu chifukwa n’kuti kumutu kwake kutachita phulusa. Anali atavala chipewa chakhonde, chomwe chingwe chake anachimanga pachigama. Chipewachi chinali chikongoletsedwa ndi kansalu kokhala ndi mikanda yamitundumitundu. Anavalanso chijasi chachikopa cha kambuku, chomwe chinali chitasosokasosoka. Chijasicho chinkamulekeza m'mawondo. Magambusi omwe anavala ankaoneka kuti akumana nazo chifukwa anali atazolowerana bwino ndi chisongole ndipo n'kuti ali ming’ankhaming’ankha. Akuyenda m'mbali mwa mtsinje uja, anaona mtengo umene ankaufunafuna. Unali mtengo waukulu wamkuyu womwe unali pakati pa chikanga china. Mtengowo unkaoneka bwinobwino chifukwa unali waukulu kuposa mitengo yonse pachikangapo ndipo ngakhale mitsitsi yake inayi, yomwe inali itatumbula nthaka, inkaoneka bwinobwino ukakhala patali. Umodzi mwa mitsitsiyo unali pakati ndipo inayo inali m'mbali. Atafika pamtengopo, anaika pansi mfuti yake ija moitsamiritsa kumtengowo kwinaku akumwetulira ndipo anasolola chikandalanga chake chomwe ankachibisa m'chijasi chija. Kenako anayamba kukumba pansi pafupi ndi m’tsitsi wapakati uja. Atamaliza, anatenga masamba ouma n'kuwaika pansi pa dzenje anakumbalo. 6