Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 69

Matigari “Taonani dzuwatu langotsala pang’ono kubira . . . Ndiku- ganiza kuti azimayiwo aweruka tsopano.” Kenako anasiya kuyenda m’kanjira kaja ndipo anayamba ku- sakasaka njira yotulukira m’mundawo. Kutuluka m’mundawu sinali nkhani yapafupi. Anayenda mtunda wautali asakudziwa kuti kumene achokera kuja n’kuti komanso asanakumane ndi aliyense yemwe akanamufunsa njira. Munda wa tiyiwo un- kangokhala ngati uli dziko lonse ndipo kulikonse komwe anka- ponya maso, ankangoona tiyi yekhayekha. Kunalibe zikwang- wani, ngakhale kwinakwake komwe kunkaoneka utsi ngati chiz- indikiro choti kumakhalidwa. Konse kunkangooneka tiyi basi. Matigari anakhumudwa. Tsikulo linali likupita kumapeto. Koma anali asanapeze akazi ake. Analinso asanaone nyumba yake. Kenako anayamba kuoneka kukalamba kwambiri chifu- kwa chokhumudwa. Ankangodzikoka moti chapatali ankayenda ngati munthu yemwe akufuna kudzipambukira. Ankayenda mokakamizika ngati wina wamuuza kuti akangoima afa. Kenako anayamba kulowera chakumadzulo. Ndiye popeza ankayenda moyang’ana komwe dzuwa linkalowera, dzuwalo li- nayamba kuwalowa m’maso. Kutentha kuja kunali kutachepa, koma kufikira pano, kunja sikunkachitabe mphepo yomwe ika- naumitsa thukuta lomwe linali noninoni pankhope zawo ko- manso lomwe linkatsetseleka kuchoka mkhwapa n’kuma- yenderera mpaka m’zigongono. Ankati akamayenda ankango- khalira kuphunthwa n’kumazula miyala ndi mapazi awo. “Koma ndiye mundawu ndi waukulu bwanji! Ndikuganiza kuti mwini wakeyo angakwanitse kukafika kumapeto pokhapo- kha atakwera hatchi.” “Kapenanso tinene kuti ndege,” Muriuki anawonjezera akuyerekezera kuuluka ngati ndege. “Ooh, ndikanakonda 68