Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 68

Matigari muno amene sakudziwa kuti apolisi akungokhalira kulimbana ndi ana asukulu komanso ogwira ntchito?” “Inde, ndi zimenetu apolisi masiku ano akumachita,” anatero Muriuki. “Kodi si dzulodzuloli limene ogwira ntchito ena anatidzimulidwa koopsa, ena anafika mpaka pothyoledwa dzipalapasiro.” “Tiyeni tikoke phazi kuti tikawapeze azimayiwo asanaweruke.” Anatero Guthera. Kenako anaima paphiri pafupi ndi chikanga china. Kutsogo- lo kwawo kunali minda ya tiyi, yomwe kumalekezero kwake sikunkaoneka. Inkangokhala ngati yopanda malire. Tiyiyo anka- duliridwa bwino zedi moti ukamamuonera patali, ankangokhala ngati kapinga. “Nthakayi ndi yachonde zedi.” Anatero Guthera. “Kodi malo onsewa ndi a munthu m’modzi?” “Inde, ngati si a munthu ndiye kuti ndi a kampani yakunja.” Ndiye popeza sankaona munthu aliyense wogwira ntchito m’mindayo, anaganiza zotsetsereka kudutsa m’tinjira tamkati mwa tiyiyo kuti awafufuze. Anayenda kwa nthawi yaitali koma sanakumane ndi aliyense mpaka anakafika kumunsi kwenikweni. Mundawo unali waukulu osati pang’ono. Muriuki anatopa n’kuyenda moti ankamva kuphwanya paliponse. Ndiyeno atayang’ana Matigari, anayamba kudabwa kuti: ‘Kodi munthu ameneyu ndi wamtundu wanji? Sindina- muone akudya chilichonse, koma sakuoneka kuti watopa nga- khale pang’ono.’ Koma atayenda mtunda wautali osafikabe kumapeto kwa mundawo, Guthera ananena kuti kuli bwino apeze malo oti agone usikuwo, ndiyeno adzapitirize kusakako tsiku lotsatira. 67