Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 66
Matigari
“Komatu mindayi ndiye ilipo yochuluka zedi, ndiye ndinga-
kayambire kuti?” Matigari anatero akukhala ngati akudziyank-
hulira yekha.
Guthera anaganizira funsolo kwa kanthawi. Kwa nthawi
yonse yomwe ankayankhulanayo, Guthera ankasakasaka mpata
woti ayamikirire zimene Matigari anamuchitira zija. Umenewu
unali mwayi wake ndipo anali ataupeza tsopano. Iye ankafuni-
tsitsa kusonyeza chiyamikiro chake kwa Matigari kaya mutu
wake umagwira kapena ayi. Mumtima anadziuza kuti: “Ndipita
nawo limodzi. Ndikawathandiza mpaka atapeza banja lawo.”
“Tiyeni ndikuperekezeni kumunda wina wapafupi.” Guthe-
ra anauza Matigari. “Ndiponso zingakhale zophwekerako kuti
ndizikafunsa ineyo chifukwa kumakhala azimayi okhaokha.”
“Tiyeni tinyamuke,” Matigari anatero akuimirira. “Tiyeni ti-
nyamuke mdima usanagwe.”
Matigari anali asanadye chakudya chake chija. Mayi
m’modzi wogulitsa mubalayo anamumangira chakudyacho
papepala. Matigari anatenga chakudyacho limodzi ndi botolo la
mowa lija n’kuzilongedza m’thumba la chijasi chake.
65