Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 64
Matigari
“N’kutheka kuti padakali pano sakudziwa mbiri yawo.
Mwina anaiwala kuti iwowo ndi ndani. Choncho ndipita
m’misika, m’mashopu komanso malo onse omwe kumapezeka
anthu, n’kukaliza mphalasa yoitana anthu onse a m’banja langa
omwe anapulumuka nkhondo. Ndikawauza kuti: Mtsamunda
Williams anafa; tsopano tiyeni tibwerere kunyumba.”
“Mtsamunda Williams ndi ndani?”
Tsopano inali nthawi yoti Matigari afotokozere Guthera mbi-
ri yake. Iye ankafunika kufotokoza mmene anaswera mphanje,
kuunda mizere komanso kudzala mbewu ndiponso mmene ana-
mangira nyumba. Pa nthawi yonseyi Mtsamunda Williams
ankangoyendayenda manja ali m’thumba, akuimba mluzu
kapena kumalamula zochita apa ndi apo. Anamufotokozeranso
zimene zinachitika atamaliza kumanga nyumbayo kuti
Mtsamunda Williams anaitenga. Anachitanso chimodzimodzi
ndi mafakitale. Matigari ndi amene ankapanga chilichonse, ko-
ma ndi Mtsamunda Williams amene ankatolera mapulofiti.
“Tangoganizani: Wolima kumafa ndi njala. Womanga kumago-
na pakhonde. Telala kumayenda mbulanda. Woyendetsa gal-
imoto kumayenda wapansi mitunda italiitali. Dziko lingakhale
lotani zimenezi zitamachitika?” Matigari anafotokozanso
mmene anayambira kulimbana ndi Mtsamunda Williams. Ko-
manso mmene John Boy anamupulumutsira. Anafotokozanso
mmene anathawira n’kupita kunkhalango komanso kumapiri
pamene Mtsamunda Williams ndi John Boy ankamuthamangi-
tsa. Anatambasuranso umo ankasakiranasakirana m’mapiri ko-
manso m’zigwa za m’dzikolo.
“Ndi dzulodzuloli limene ndamuchotsa chimbenene.
Atagwera pansi, ndinapita n’kukamuponda pachifuwa. Kenako
ndinakweza zida zanga m’mwamba n’kuyamba kuimba nyimbo
63