Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 63

Matigari “Sindinaonepo apolisi akuteteza anthu.” Guthera anatero. “Tangoganizira mmene zinakhalira ndi bambo ako, munthu wokonda dziko lake. Munthu wotumikira ena! Palinso mitundu iwiri ya anthu m’dzikoli: Pali amaliwongo ena omwe amaligu- litsa, ndipo ena amayesetsa kuthandiza anthu. Amenewa ndi an- thu okonda dziko lawo.” “Dzina lanu ndi ndani?” “Matigari ma Njiruungi.” “Ndinu m’modzi wa anthu omenyera ufulu wa dziko? Kodi ndinu m’modzi mwa anthu omwe anatsala kunkhalango kuti moto wa ufulu wathu usazime? Mwachokera kuti?” “Ndabwera kuno m’mawawu kuchokera kumapiri.” “M’mawawu? “Inde, ndabwera kuno m’mawa womwewu ndithu.” “Ndiye mnyamatayu ndi ndani wanu?” Guthera anafunsa akutembenukira kwa Muriuki. “Ndinakumana naye pafupi ndi kumtaya,” anatero Matigari. “Zoona?” Guthera anafunsa akuyang’ana Muriuki. “Kodi ndiwe m’modzi wa ana omwe amakhala kumanda a galimoto aja?” “Inde,” Muriuki anatero. “Ndiye kubala kuno mukudzataniko?” Guthera anafunsano Matigari. “Ndiye kuti mulibe wachibale kapena nyumba yoti mungakafikireko eti?” “Ndikufufuza anthu anga kuti tipitire limodzi kunyumba kwathu.” “Anthu ake aja ankamenyera ufulu wa dziko lathu, omwe anapulumuka pa nkhondo?” 62