Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 62
Matigari
umakuotcha ndi mkute wadzulo! Mvula ikakuona litsiro sikata.
Anthuwo atangomuona, onse analikumba liwiro. Ankati:
“Mwana wachigawenga ujatu ndi ameneyu! Tikachita masewera
tikhoza kuputa naye mavuto.” Nthawi zonse ankati akapita
kutchalitchi ankabwerako chimanjamanja.”
“Tsiku lina, mtsikanayo anaganiza zoyamba kuyendayenda
m’tauni. Tsiku limenelo anabwera ndi kawokomani ka ufa.
Ndikufuna kukutsimikizirani kuti: Kungoyambira tsiku li-
menelo, anayamba kupeza zakudya komanso zovala za abale
ake aja. Koma sankapeza ndalama zokwanira kuti akanawa-
tumiza kusukulu kapena malo ena omwe akanapita kukapalira
tsogolo lawo pophunzira maluso osiyanasiyana.” Si pano ndi
awo ndimakumana nawo m'mabala komanso m'mashopu aku-
dya zotoleza m'mabini komanso akupempha azungu kuti
awathandize m'misewumu? Nkhani yanga yathera pamenepa.
Koma mwina sindinayankhebe funso lanu. Kungochokera tsiku
limene mtsikanayo anayamba uhule, analumbira kuti: ‘Ngakhale
kuti mavuto ndi amene achititsa kuti ndisiye kuyenda m'njira
yachiyero n’kukhala hule, sindidzayerekeza kuyenda ndi wap-
olisi. Ndizichita uhule ndi anthu ena omwe sindikuwadziwa
monga akuba komanso zigawenga. Koma sindidzayerekeza
kuyenda ndi anthu oipa mitima amenewa, ngakhale atandilonje-
za kuti andipatsa thumba lamakobidi.’ Anasankha kuti awonje-
zere lamulo limeneli pamwamba pa malamulo khumi aja.
“Pali Akhristu a mitundu iwiri,” anatero Matigari ndipo
zimene ananenazo zinadulako bata lomwe linali pamalopo pam-
buyo poti Guthera wamaliza kunena mbiri yake ija. “Ena ama-
konda dziko lawo, pomwe ena amaligulitsa. Palinso mitundu
iwiri ya asilikali. Ena amateteza anthu, koma ena amawazunza
komanso kuwapha.”
61