Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 61
Matigari
zida. Munthu amene wapezeka ndi zipolopolo popanda laisensi
amayenera kunyongedwa. Koma ineyo ndikufuna ndikuthan-
dize. Palibenso munthu wina kunja kwa polisi ino amene akud-
ziwa za nkhaniyi. Ukangovomera kuti ugona ndi ine, timasula
bambo akowa. Koma mtsikanayo anamenyetsa nkhwangwa
pamwala. Iye anayankha kuti: ‘Sindingachite zinthu zomwe zin-
gakhumudwitse atate wanga wakumwamba. Iye anapereka
lamulo lakuti: Usachite chigololo.’ Koma wapolisiyo anamuuza
kuti: ‘Basitu, bambo ako wawapereka kuti akaphedwe, moti
sudzawaonanso.’ Kenako bambo ake aja anaphedwadi. Malo
awo analandidwa ndi boma ndipo mtsikanayo anatsala ndi
chiudindo chosamalira abale ake aja. Kenako mavuto anayamba
kuunjikana. Umphawi, usiwa komanso chakudya chinkasowa.
Analibiretu chilichonse. Ana ena aja anayamba kulira kuti: ‘Kodi
bambo ali kuti? Kodi lero tidya chiyani?’ Mtsikanayo
ankangowayang’ana akusowa chonena. Iye ankati akaganizira
kuti akanatha kupulumutsa bambo ake, ankadziimba mlandu
kwambiri. Ankati akamva abale ake aja akulira ndi njala, mtima
wake unkamupweteka zedi. Ankadziuza kuti: ‘Kodi tsopano
ndizingoonerera abale angawa akufa ndi njala? Ndaphetsa kale
bambo anga, kodi ndilolera kuti ndiphetsenso abale angawa?
Nkhani imeneyi inkamuzunguza mutu kwambiri. Koma atate
wake wakumwamba sankayankha mafunso akewa. Zimene Bai-
bulo linkanena zinali zoti: Usabe. Usasirire . . . kanthu kalikonse
ka mnzako. Usachite chigololo. Koma kunena za njala, yankho
panalibe. Nanga bwanji za ludzu? Yankho panalibenso. Nanga
bwanji usiwa? Ayi ndithu. Ndipo kunyumba ana ankangokha-
lira kulira: ‘Njala ikuwawa! Kodi bambo abwera liti? Kodi anapi-
ta kuti?’”
“Mtsikanayo anapitanso kwa wansembe uja. Iye anapempha
anthu a m’tchalitchicho kuti amuthandize. Koma tsoka likalimba
60