Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 60
Matigari
‘Inde ndi zoona. Palibe chikondi chachikulu ngati ichi: kuti
amuna ndi akazi apereke moyo wawo m’malo mwa anthu am-
biri popita kumapiri komanso nkhalango. Limeneli ndi lamulo
lalikulu kwambiri m’chilamulo cha Khristu, komanso ngakhale
kwa Muhammad ngakhalenso Buddha.’ Mtsikanayo anazizidwa
thupi atamva zimenezi moti kwa kanthawi anangokhala khuma.
M'masiku amenewo kupezeka ndi zipolopolo unali mlandu wo-
ti munthu ankanyongedwa nawo. Kenako mkulu wa apolisi uja
anabweranso n’kutenga bambo ake aja n'kukawatsekera. Posa-
khalitsa anatulukiranso, akumwetulira mwaudyabolosi. Iye
anati: ‘Akuboma sindinawauze za nkhaniyi. Nkhaniyi tikhoza
kuithetsa ngati iwe ndi ine titagwirizana. Ngati utavomera kuti
ugona ndi ine, bambo akowa tiwatulutsa.’ Mtsikanayo sa-
nayankhe kanthu. Mkulu wa apolisiyo anapitiriza kuti:
‘Ukudziwa kuti moyo wa bambo akowa uli m'manja mwako?”
“Mtsikanayo anabwerera kunyumba ndipo atafika anazika
maondo pansi n’kupemphera kwa atate wake wakumwamba
n’kumupempha kuti amupatse nzeru komanso kumutsogolera.
Tsiku lotsatira anapita kwa wansembe. Wansembeyo anatsegula
Baibulo n’kumuwerengera Malamulo Khumi. Iye anati: Usakha-
le nayo milungu ina koma Ine ndekha. Usaphe. Usachite
chigololo. Uzilemekeza atate wako ndi amako . . . Kenako anati,
‘Pamenepa ndi pamene pagona chiyeso. Lamulo lina likuti,
Usaphe. Lina likuti, Usachite chigololo; pomwe lina likuti, Uz-
ilemekeza atate wako ndi amako . . .” Kenako onse anagwada
pansi n’kupemphera. Wansembeyo anapemphera kwa Mulungu
kuti apereke nzeru kwa mtumiki wake, kuti apitirizebe kuyenda
m’njira yachiyero. Tsiku lotsatira, mtsikanayo anapitanso
kupolisi kuja. Mkulu wa apolisi uja anabwerezanso kumuuza
kuti: ‘Bambo akowa ali m’gulu la anthu omenyera ufulu wadzi-
ko lawo. Ndipo agwidwa akuthandiza zigawenga pozipatsa
59