Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 6

Matigari Gawo 1 M'dzanja lake lamanja munali mfuti ya AK47. Dzuwa n'kuti likukwera ndipo kuti lisamulowe m’maso, ankagwiritsa ntchito dzanja lake lamanzere popherera cheza chake. Pa nthawiyi n’kuti ali m’mbali mwa mtsinje ndipo tsidya lina la mtsinjewo ndi lomwe linakola chidwi chake. Aka sikanali koyamba kuchita zangati zimenezi. Kwa zilumika zosawerengeka, ankadutsa akujodimajodima m'mapiri komanso m’zigwa za m’derali, ndipo anali atazungulira ngodya zonse za dziko lapansi. Nkhondo inali itafika kumapeto tsopano. Komabe, ankadziwa kuti akufunika kumagona diso limodzi lili lotsegula. Posakhalitsa hatchi ina inadutsa chapafupi ili jidimujidimu. Hatchiyo inaima, n'kumuyang'ana kwa kanthawi ngati ikumudziwa. Kenako inalowa m'zikanga n'kuzimiririka. Hatchiyo inamukumbutsa Mtsamunda Williams komanso anzake omwe ankakonda kukwera mahatchi akamapita kokashomola nkhandwe, agalu awo onenepa ali tawatawa kuwatsatira. Zimenezi zinachititsa kuti maganizo ake abwerere padzana. Mtsamunda ameneyu anali ndi ludzu la magazi osati pang'ono! Nthawi zambiri ankakonda kuvala zofiira, n'kutengana ndi anzake kupita kukasaka ali pamsana pamahatchi. Munthu woyambirira kupha nkhandwe ankaidula mchira akusangalala, ndipo ankakadzodza magazi ake pamphumi pa mkazi wake. Ndithu, panalidi patadutsa zaka zambiri asanaonenso zangati zimenezi zikuchitika. Akakumbukira nthawiyo, iye ankavomereza kuti mdima ungakule, usiku ungatalike bwanji, koma kunja kumacha basi! Iye ankakhulupirira kuti mavuto onse omwe ankabwera chifukwa cha ulamuliro wachitsamunda atha tsopano. 5