Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 59
Matigari
“Choncho, iye anabadwanso mwatsopano. Anayamba kuta-
manda Mulungu modzikhuthula, moti nthawi zina ak-
amapemphera ankadzimva ngati wamera mapiko n'kuulukira
kumwamba. Koma kenako nkhondo inayambika. Nkhondoyo
inachititsa kuti anthu ayambe kugawikana. Ena anakhala ome-
nyera ufulu wawo, pomwe ena anayamba kulimbana ndi ome-
nyera ufuluwo. Dzikoli linangotembenukiratu. Ana anayamba
kuukira makolo awo, makolonso anayamba kulimbana ndi ana
awo. Atsikana komanso anyamata apachibale analumbira kuti
apha abale awo. Koma mtsikanayo anatsimikiza mtima kuti
azimvera anthu awiri okha pamoyo wake: Atate ake akumwam-
ba komanso apadziko lapansi. Iye ananenetsa kuti adzachita
chilichonse chotheka kuti azichita zokondweretsa atate ake awir-
iwa. Bambo ake ankapita kutchalitchi sabata ndi sabata. Koma
nawonso anali womenyera ufulu wadziko lawo. Mtsikana uja
sankadziwa zimenezi. Nthawi zosawerengeka bambo akewo
ankamuuza kuti: ‘Malamulo khumi onsewa ndi abwino, koma
onsewa agona palamulo limodzi: Chik o nd i. Ndipo palibe
chikondi choposa ichi: kuti munthu apereke moyo wake
kuwombola anthu ambiri. Tangoganiza, anthu onse atakhala
okonzeka kupereka moyo wawo m'malo mwa anthu ena, ko-
manso m’malo mwa dziko lawo.’ Tsiku lina bambo ake apadziko
lapansi aja anamangidwa. Apolisi anamuuza mtsikana uja kuti:
‘Bambo ako anapezeka atanyamula zipolopolo m’Baibulo.’ Mtsi-
kanayo anakana kuti bambo ake akuwadziwa bwinobwino, ndi
munthu wabwino moti sangachite zimenezo. Koma mkulu wa
apolisiwo anamuuza kuti, ‘Dikira tiwabweretse kuti uwafunse
wekha.’ Kenako anabwera nawo unyolo uli m’manja. Mtsi-
kanayo ataona bambo akewo, anagwetsa misozi. Kenako wap-
olisi uja anachokapo kaye. Iye anawafunsa bambo ake aja kuti,
‘Zimene akunenazi ndi zoona?’ Bambo akewo anayankha kuti,
58