Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 58
Matigari
anthu awiri pamoyo wake: Atate ake wakumwamba omwe ana-
mupatsa moyo komanso atate ake apadziko lapansi omwe
ankamulera mwachikondi kwambiri. Atate ake apadziko
lapansi ankakonda ana awo zedi. Iwo sankadya chakudya
pokhapokha aonetsetse kuti ana onse akhuta. Iwo sanka-
kondera mwana aliyense. Kwa iwo ana onse anali ana ochokera
kwa Mulungu, zolengedwa zake, ndipo onse anali ofanana.
Ngakhale anali osiyana ngati zala za m’manja, onse ankafunika
kusamaliridwa mofanana. Mtsikanayo sankalephera kupita
kutchalitchi ndiponso kupemphera kwa Mulungu wake. Ali
kutchalitchiko, anaphunzira Malamulo Khumi. Koma atakula
anayamba kuwerenga yekha malamulowo. Iye anaphunzitsid-
wa kuti azisunga malamulo amenewa nthawi zonse, kulikonse
kumene ali, kaya ena akumuona kapena ayi.”
Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha.
Usadzipangire iwe wekha fano losema.
Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe.
Uzikumbukira tsiku a Sabata, likhale lopatulika.
Uzilemekeza atate wako ndi amako . . .
Usaphe.
Usachite chigololo.
Usabe.
Usamnamizire mnzako .
Usasirire . . . kanthu kalikonse ka mnzako.
“Cholinga chake chachikulu chinali choti asamachite zoipa.
Iye ankafuna kumachitira ena zinthu zabwino. Ankafuna
kutsatira njira ya chilungamo komanso kukhala ndi khalidwe
loyera.”
57