Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 57
Matigari
wina kuti amwe.”
Onse anakhala n'kumamwa zakumwa zawo ndipo palibe
ankayankhula. Ngakhale azimayi aja ankayankhula motsitsa
mawu kwambiri ngati akuopa kuti wina awatapa m’kamwa.
“Chinachitika n'chiyani kuti apolisiwa azilimbana nawe
chonchi?” Matigari anafunsa Guthera.
Guthera anakhala ngati akukayikira kuti ayankhe kwinaku
akuyang'ana Muriuki. Zinkakhala ngati sakufuna kufotokoza
Muriuki ali pomwepo. Koma kenako anaganiza zotambasura
nkhani yonse.
“Nkhani imeneyi sindinayambepo ndauza munthu,”
anayamba motero. “Mungachite bwino kudzifunsa kuti n’chifu-
kwa chiyani ndimapezeka kubala kuno? Dikirani ndkuyalireni
zonse zomwe ndakumana nazo pamoyo wanga.”
“Kalekalelo, kunali mtsikana wina wodzisunga. Mayi ake
anamwalira pamene mtsikanayu ankabadwa. Mtsikanayu
limodzi ndi azichemwali komanso azichimwene ake, an-
aleledwa ndi bambo awo achikondi. Bambowo anali Mkhristu
wokonda kupemphera ndipo anali mkulu wampingo. Mtsi-
kanayo nayenso anakula akuopa Mulungu. Iye ankapita ku
Church of Scotland pomwe bambo ake ankapita ku Independent
Church. Chochititsa chidwi n’choti bambo akewo sankamuletsa
kupemphera tchalitchi china. Iwo ankati chofunika kwambiri
ndi kutsatira Mawu a Mulungu komanso malamulo ake ndipo
ankaona kuti chipembedzo sichidzapulumutsa munthu, koma
mtima. Iwo ankati chipembedzo cholondola chili mumtima.
Mawu omwe sankachoka pakamwa pawo anali akuti
matchalitchi angokhala nyumba zomwe anthu amakumanamo
kuti alambire Mulungu. Mtsikanayo ankakonda kwambiri
56