Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 56
Matigari
Gawo 10
Matigari ndi Muriuki anabwerera kubala ija. Azimayi aja
anali akukambirana zomwe zinali zitangochitikazo. Iwo ankati:
“Sitinayambe taonapo munthu wolimba mtima chonchi!” Mayi
wina anapita kukatsegulira Matigari botolo la mowa.
“Mubweretsereni Muriuki botolo lina la Fanta,” Matigari
anauza mayi uja.
Iye anangokhala duu, osadya kapena kumwa. Maganizo
ake anali patali.
Kenako Guthera analowa mubala ija. Tsopano anali atasam-
ba, atasintha zovala zake komanso atavala kampango kena.
Azimayi aja anamuthamangira n'kukamukumbatira ndipo ana-
mupepesa chifukwa cha zimene zinachitikazo. Kenako
anachoka panali azimayiwo n'kupita kwa Matigari. Iye anaima
mwaulemu pafupi ndi Matigari. Pamene ankayankhula
zinkamveka ngati akuyankhula mwamantha.
“Sindikudziwa kuti ndinu ndani . . . Koma ndikupempha
kuti mundikhululukire chifukwa cha zonse zomwe ndinanena
zija. Sindidzaiwala zomwe mwandichitira lerozi kwa moyo
wanga wonse.”
“Khala pansi,” Matigari anatero. “Ukhoza kuitanitsa botolo
la mowa wakumtima kwako kuti ukonkheko kukhosi. Kunjaku
kukutentha zedi.”
Guthera anakhala moyang'anizana ndi Matigari komanso
Muriuki. Kenako anaitanitsadi mowa. Muriuki nayenso anai-
tanitsa Fanta wina. Mayi ankawabweretsera zakudya uja ana-
mubweretseranso Matigari botolo lina la mowa.
“Inetu ndimafunatu botolo limodzi basi,” Anatero Matigari.
“Komabe ingolisiyani patebulo pomwepa, mwina tipatsa
55