Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 54

Matigari “Tayerekeza ngati ukufuna kuona chimene chinameta nyani mduliro! Mwina sukudziwa bwinobwino munthu amene uku- limbana naye.” “Kodi ndinu ndani?” wapolisi wina uja anafunsa. “Matigari ma Njiruungi.” Matigari anali atasinthiratu moti ankangokhala ngati si yemwe uja. Kulimba mtima kwake kunachititsa kuti makwinya komanso mizere yatsinya inali pankhope ija ibalalike ndipo ankangooneka ngati kamnyamata kachisodzera. Wapolisi anagwira galu uja anayamba kuchita zinthu ngati akufuna kumasula galuyo. Koma mnzake uja anamunong'oneza: “Bwanawe, tiye tidzipita. Kodi unayamba wamvapo munthu wa dzina ngati limeneli? Mwinanso akhoza kukhala wochokera kulikulu lathu. N’kutheka wabwera kuti adzaone mmene timag- wirira ntchito. Enatu akumadzisintha kuti aoneke ngati anthu wamba! Iwe ukuganiza kuti chikumulimbitsa mtima n’chiyani? Munthu ameneyutu waponda mwala!” “Wewe mwenda wazimu,”* wapolisi anali ndi galu uja anatero kwa Matigari. ‘Ndiponso mtsikana iwe, uyenera kumamvera an- thu omwe apatsidwa udindo woonetsetsa kuti m'tauni muno muli bata ndi mtendere.’” *Wewe mwenda wazimu (Kiswahili): Kutanthauza “Wamisala iwe eti!” Apolisiwo anachoka pamalowo n'kumalowera kunali mashopu omwe anali m’nyumba yansanjika ija. Matigari anapita panali mtsikana uja ndipo anamugwira paphewa. “Basi imilirani mayi wanga.” Matirani anatero mwachifundo. Guthera anali akunjenjemera ndi mantha. Anaimirira mwapang'onopang'ono ndipo kenako anatola mpango wake uja n’kunyamuka kumapita. Zimene zinachitikazi sizinachoke 53