Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 53

Matigari azikulamulirani? Pajatu akuluakulu anati, mantha amabala mavuto ambiri m'dziko.” Pa nthawiyi maso onse anali pa Matigari. Kenako gulu la an- thulo linayamba kufutuka n’kugawika pakati ngati mmene zimakhalira anthu akamapisa wamisala kuti adutse. Matigari anadutsa pakati pa gululo ndipo sanasithe sitepe yake. Kenako anatukula mkono n'kuloza apolisi aja. Ndiyeno anawauza kuti: “Tamusiyani mtsikanayo nsanga!” “Ndi ndani amene wakupatsani udindo woti muzilimbana ndi lamulo?” wapolisi ankakoka galu uja anafunsa motero. “Ndi lamulo lake liti limene limalola apolisi kumazunza mtsikana wosalakwa?” Wapolisiyo anayamba kuchita mantha, chifukwa sankadziwa kuti munthu amene akulimbana nayeyo ndi ndani komanso kuti chikumulimbitsa mtima n’chiyani kuti aziyankhula motero. “Kodi mukudziwa kuti mtsikana ameneyu sanamvere apoli- si atauzidwa kuti aime? Ife tili pano kuti tionetsetse kuti pa- malowa pali bata ndi mtendere,” wapolisi anali ndi galu uja anatero. “Bata ndi mtendere wake uti? Mukulimbana ndi mtsikanayu apa n’kumalekerera atsinzinamtole ndiponso mbava zikuluziku- lu zakuba momasuka? Bwanji osangovomereza kuti muku- muzunza chifukwa choti akukukanani?” “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni galuyu?” wapolisi uja anafunsa mwamanyazi akuoneka wanyowa, Matigari atamuya- lutsa pagulu. “Mukufuna kuti ndikumasulireni galuyu kuti akukhadzu- leni? Ndikhoza kumusiyatu! Mwapepetulidwa eti? Kapena mwatopa nawo moyo?” 52