Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 52
Matigari
Nthawi iliyonse imene Guthera ankadzuka kuti athawe, galuyo
ankamulumphira, kwinaku akuuwa mochititsa mthumanzi ko-
manso akubangula ngati wamva fungo la magazi. Anthu ena
ankangoseka, ndipo zinkaoneka kuti zimene zikuchitikazo
zinkawamaliza koopsa.
Kenako nkodzo unayamba kuyenderera pamiyendo ya
Guthera. Ankachita mantha kwambiri chifukwa ankaganiza kuti
galuyo amukhadzulakhadzula basi.
Matigari ataona izi mtima wake unamuwawa zedi. Ankango-
khala ngati wina akumukolokosa pachilonda. Anayendetsa
manja m'chiuno mwake ngati mmene ankachitira pa nthawi
yonse yomwe ankalimbana ndi Mtsamunda Williams kumapiri
kuja. Koma sanapezemo kalikonse. Iye analibe mfuti yake.
Tsopano anakumbukira kuti anali atavala lamba wamtendere.
Koma anali atanyangala ndi nkwiyo woopsa. Iye anadzifunsa
kuti: “Ndi munthu wamtundu wanji yemwe amalephera kute-
teza ana ake?” Komabe sikuti anangoutsekera mkwiyowo
mumtima. Nthawi zonse ankadziuza kuti palibe chifukwa
chokwiyira ndi zinthu ngati sukufuna kuchitapo kathu kuti
uzisinthe. Kenako anauza gulu la anthu aja mokwiya kuti:
“Kodi chikuchitika n'chiyani apa? Anthu akuluakulu ngati
inu mungangoima pamenepopo muli ndevu pepeyaa, n'ku-
maonerera mwana wanu akudyetsedwa matudzi ndi anthu oipa
mitimawa? Zoona makosana nonsenu mungamagwedezere mitu
n'kumavomereza kuti anthu ankhanza azizunza ana osalakwa?
Ndi usiwa wam’maganizo wamtundu wanji womwe
wakugwirani kuti muzingoonerera mtsikana wokongola ngati
uyu akupondedwapondedwa ndi chilombo?”
“N'chiyani chikukuseketsani pamenepa? N'chifukwa chiyani
mumadziphimba ndi nsalu ya mantha, n'kulolera kuti mantha
51