Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 51

Matigari mizere yambatata. Ankadziuza kuti, “Koma ndiye zinthu zasin- thatu! Kodi dzikoli likulowera kuti abale inu? Si malodza ame- newa?” Azimayi anali pogulitsira mowa aja anayamba kukamba za Guthera. “Guthera ndi woyerekedwa komanso wapakamwa kwabasi. Sindidziwa chifukwa chimene amakanira apolisi. Ndalamatu siluma! Ineyo ndikanakhala Guthera, ndi- kanamawatsata kwambiri apolisiwo kuti atulutse tindalama tonse tomwe ali nato mpaka afike popinyoletsa yunifomu yawo.” Anapitirizabe kukamba za Guthera kuti angowonon- gako nthawi. Kenako anangomva kulira koopsa kwa galu ndipo kulirako kunangotsagana ndi kulira kwa mtsikana. Azimayi aja anasiya zonse zomwe ankachita n’kuthamangira panja ndipo nayenso Muriuki anatuluka. Galu uja anapitirizabe kuuwa moopseza. Mtsikanayonso ankalira mosatonthozeka. Muriuki anabwerera mubala ija akunjenjemera ngati wodwala malungo. “Ndi, ndi, ndi mtsikana uja!” anatero Muriuki. “Watani?” “Akufuna kumulumitsa galu.” “Ndani?” “Apolisi.” Matigari anadzambatuka pampando womwe anakhala n'kuthamangira panja ndipo Muriuki ankamutsarira pambuyo. Iye sanakhulupirire zimene anaona panjapo. Gulu la anthu linali litazungulira n’kumaonerera apolisi aku- khaulitsa mtsikana. Guthera anali atagwada pansi ndipo galuyo, yemwe ankakokedwa ndi wapolisi, ankamulumphira kuti amu- lume. Kansalu kake kankhosi kaja kanali katagwera pansi. 50