Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 49
Matigari
anatero ndipo pamene ankayankhula anatembenuka n’kuona
Matigari ndi Muriuki. “Bolanso kupempha mowa kwa munthu
amene sindikumudzidwa, ngati bambo akhala apowo.”
Guthera anachoka panali anzake paja n’kupita kumene
kunali Matigari ndipo mosachedwachedwa anamukhalira
pamiyendo n’kukoloweka mikono yake m’khosi mwa Matigari
akumuyang’ana ndi diso lachikondi.
“N’chifukwa chiyani mukundiyang’ana choncho dadi?
Mukuonekansotu kuti mwaiwala kudya chakudya komanso
kumwa mowa wanu. Ine ndimamwa mowa wangati juwisi
womwewu. Sindikonda zitsulo. Uum! Musanyade, monga
simundigulira umodzi? Ngatinso mukufuna zina ndi zina
ndikhoza kukutchipitsirani. Muli ndi zingati? Anthu enatu ama-
dulitsa, mukudziwa? Koma popeza pano ndi pakati pa mwezi,
iliyonse yomwe munthu ali nayo timalandira. Ndipo nthawi zi-
na timatha kulola ngongole. Mukhoza kudzandipatsa mwezi
ukatha. Koma ndimalola zimenezi pokhapokha ngati munthu ali
pantchito. Muli pantchito eti? Kapena mumachita ulimi
wang’ombe zamkaka? Kapena muli ndi munda wakhofi?
Mukhozanso kukawaponda akazi anu ndalama zomwe agulitsa
tomato kunsika lero. Musadandaule, ife bola munthu atipatse
chilembwe basi, sitilabada kaya zachokera kuti. Koma nthawi zi-
na timakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, ngati ogwira ntchi-
to atachita sitiraka, sindikudziwa kuti ndipeza kuti ndalama zo-
gulira chakudya. Masiku sakoma onse, lero umati kuseka, mawa
kulira. Komabe sitimataya mtima chifukwa nthawi zina azimu
amatha kutigwera m’mbale. Timatha kukumana ndi azibambo
omwe agulitsa malo. Kodi nanunso muli ndi malo? Mukhoza
kugulitsa ngakhale a mkazi wanu, mukhozanso kugulitsa nga-
khale nyumba yake. Mukagulitsa eti da?”
48