Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 48
Matigari
Gawo 9
“Bwanji? Waba chiyani?”
“Ayi, sindinabe kanthu. Kungoti wapolisi wina amandifuna.
Akumangokhalira kunditsata ngati ntchentche. Kaya akuganiza
kuti ndikumufuna. Akanakhala wanzeru akanachita manyazi.
Eti kumandiimbira likhweru n’kumandiuza kuti ndiime. Ndani
wamisalayo yemwe angaime n’kumacheza ndi wapolisi dzuwa
likuswa mtengo! Ndiyetu akam’fune wosewera naye. Munthu
wake si ine ayi!”
Matigari atamuona Guthera, anaona kuti mtsikanayo ndi
njole yeniyeni, chiphadzuwa. Mano ake anali oyera ngati mkaka,
tsitsi lake linali lambiri, lakuda bwino komanso lofewa.
Zinkangokhala ngati nthawi zonse amalipaka mafuta a mtsatsi.
Iye sanali wamtali komanso sanali wamfupi. Sanali wonenepa
komanso sanali woonda. Zimene anavala zinkamukhala ngati
analengedwera momwemo. Khosi la Matigari linakhala ngati
latha girisi chifukwa linkakanika kutembenuka n’kuchotsa maso
kuchoka kumene kunali mtsikanayo. Mumtima mwake ankati,
“Tangoonani kansalu kokongola kali yaliyali paphewako.”
Kansaluko kanali katagwera pachifuwa. Sinali nkhani ya-
masewera kuchotsa diso lake pa mtsikanayu. Analidi mtsikana
woika pachiyeso ngakhale m’busa yemwe analumbira kuti
sadzapenyetsetsa namwali. Ndani ananena kuti nawonso abusa
alibe maso. Maso alije mpanda. Komabe Matigari ankadzifunsa
kuti, “Kodi mtsikana wokongolayu akudzataniko kubala kuno?”
Kenako azimayi aja anagundika nako kuseka.
“Apolisiwo atani Guthera? Sumawakonda? Ndalamatu ndi
ndalama, sitimalabadwa kuti zachoka kuti.”
“Ineyo ayi. Ndalama za apolisi zimanunkha magazi,” iye
47