Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 47

Matigari Pamene ankaganizira zoti achite, anangoona mtsikana wina watulukira ndipo mtsikanayo atalowa anapita pomwe panali azimayi aja. Analonjerana nawo powapatsa moti wathabwa kwinaku akusangalala kwambiri. “Uli bwanji Guthera,” onse anapatsana moni. “Mwamva zotani anzathu?” “Palibe,” anayankha motero akumwetulira. “Kungoti ndikuzemba apolisi enaake. Sindikufuna ndikumane nawo.” Mayi anali pogulitsira zinthu uja anatsitsa voliyamu ya wailesi ija kuti amve bwinobwino zimene Guthera ankanena. 46