Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 46

Matigari Matigari anapita kukakhalanso patebulo paja ndipo anamupeza Muriuki atatanganidwa kwambiri ndi kugalika zakudya zake. Atakhala pansi, ankangoyang’ana chakudya chake chija ngati sakuchifuna, moti sanachikhudze ngakhale pang’ono. Iye ankangodzifunsa mafunso ambirimbiri. Ankaganizira za Muriuki komanso anthu ake onse. Pamene ankatuluka munkhalango muja, ankaganiza kuti kusonkhanitsanso anthu a m’banja lake kukhala kophweka. Koma tsopano zinkaoneka kuti ntchito ilipo. Dzuwa linali litayamba kupendeka, ndipo anali asanakumane wachibale wake ngakhale m’modzi. Sankadziwanso kuti ayambira pati kuwasakasaka. Kenako azimayi aja anatsegula wailesi. . . . Mwatsegulayi ndi Wailesi Yanu ya Choonadi. Tsopano timvetsera pulogalamu ya azimayi. Lero tikambirana nkhani zokhudza banja . . . Msonkhano wapachaka wa Chitukuko cha Amayi unatseguliridwa ndi mkazi wa Nduna Yoona Zachilungamo dzulo. Mkazi wa ndunayo anauza azimayi kuti kuchita chigololo komanso kumwa mowa n’kumene kukuchititsa kuti mabanja ambiri apasuke m’dziko muno. Mayiwo analimbikitsa akazi onse kuti azilimbikira kupemphera komanso kuti asiye kupikisana ndi amuna awo pa nkhani ya kumwa mowa komanso kuchita chiwerewere. Iwo anati mzimayi ndi munthu wofunika kwambiri pakhomo ndipo ndi amene angachititse kuti banja lake liziyenda bwino. Kenako Matigari anati: “Zoonadi mayi ndi wofunikadi pakhomo. N’chifukwa chiyani sindinaganize zimenezi poyamba paja? Ndikanayamba ndi kufunafuna mayi kaya! Ndiyeno ndikapeza mayi, andiuza kumene kuli ana. Mayi ndi amene amasunga mtundu komanso kusamalira malo.” 45