Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 45
Matigari
moto uja unakolera nyumba yonse moti mayi anga anapsera
momwemo.”
Matigari anaingitsa ntchentche yomwe inkauluka pafupi ndi
khutu lake. Ntchentcheyo inkangokhala ngati yatumidwa. Itaona
kuti ikhoza kuonetsedwa zakuda, inathawa n’kuzungulira
kangapo kenako inakatera pafupi ndi zenera. Matigari ataona
kuti yatera, anatembenuka n’kuyang’ana Muriuki. Mumtima
mwake ankangoti: “Kodi idzafika nthawi pamene ana amasiye
adzapukute misozi yawo n’kuyamba kuimba lokoma?”
Mayi uja anawabweretsera chakudya komanso zakumwa
zomwe anaitanitsa. Zitangoikidwa patebulo, Muriuki anayamba
kutsopa botolo lake la zakumwa zoziziritsa kukhosi.
“Botolo langalo musalitsegule,” anatero Matigari. Kenako
anaimirira n’kupita kukasukusula pampope wina womwe unali
pafupi ndi chimbudzi. Magazi omwe anali pankhope yake
anayamba kusungunuka ndipo ankachititsa kuti madzi amene
ankakhera pansi azioneka ofiira. Atamaliza kusukusulako,
anapha ludzu lake pomwa ndi dzanja lake madziwo mofanana
ndi mmene imachitira ngamila yaludzu.
Mayi anawabweretsera zakudya uja anabwerera komwe
kunali mnzake uja ndipo anakakhala pansi. Azimayiwa
anapitiriza kukambirana nkhani ya sitiraka ija. Mabotolo awiri a
theka anali patsogolo pawo. M’modzi wa aziyiwo ankaluka
mosonyeza kuti anazolowerana nazo kwambiri moti zinkaoneka
kuti ankachita zimenezo asakuganiza n’komwe. Ndiyeno mayi
ankalukayo anauza anzake onse kuti: “Tiyeni timvetsere
pulogalamu ya azimayi ija. Nthawi yake yangokwana kumene.”
Kenako anadzuka n’kupita kukachotsa nyimbo inkalira ija.
44